Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 18:5 - Buku Lopatulika

5 Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israele; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israele; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Hezekiyayo adakhulupirira Chauta, Mulungu wa Aisraele, kotero kuti panalibe wofanafana naye pakati pa mafumu onse a ku Yuda iyeyo atafa, ngakhale pakati pa amene analipo kale iye asanaloŵe ufumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Hezekiya anadalira Yehova Mulungu wa Israeli. Kotero panalibe wina wofanana naye pakati pa mafumu onse a Yuda, asanakhale mfumu kapena atakhala kale mfumu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 18:5
20 Mawu Ofanana  

Nanena nao kazembeyo, Muuzetu Hezekiya, Itero mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya, Chikhulupiriro ichi nchotani uchikhulupirira?


Muzitero naye Hezekiya mfumu ya Yuda, kuti, Asakunyenge Mulungu wako amene umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya Asiriya.


Ndipo asanabadwe iye panalibe mfumu wolingana naye, imene inatembenukira kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu yake yonse, monga mwa chilamulo chonse cha Mose; atafa iyeyu sanaukenso wina wolingana naye.


Ndipo Asa anafuulira kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, tatulukira aunyinji awa m'dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakukanikeni.


Nalawira mamawa, natuluka kunka kuchipululu cha Tekowa; ndipo potuluka iwo, Yehosafati anakhala chilili, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala mu Yerusalemu, limbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzalemerera.


Zitatha izi, Yehosafati mfumu ya Yuda anaphatikana ndi Ahaziya mfumu ya Israele, yemweyo anachita moipitsitsa;


Angakhale andipha koma ndidzamlindira; komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pake.


Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu.


Koma ukanena kwa ine, Ife tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; kodi si ndiye amene Hezekiya wachotsa misanje yake ndi maguwa ake a nsembe, nati kwa Yuda, ndi kwa Yerusalemu, Inu mudzapembedzera patsogolo pa guwa la nsembe ili?


Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndachita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.


Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.


kuti ife amene tinakhulupirira Khristu kale tikayamikitse ulemerero wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa