Yeremiya 17:18 - Buku Lopatulika18 Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la choipa, muwaononge ndi chionongeko chowirikiza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la choipa, muwaononge ndi chionongeko chowirikiza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Koma ondizunza ndiwo achite manyazi, osati ineyo. Ade nkhaŵa ndi iwowo, osati ineyo. Tsiku la tsoka liŵafikire, ndipo muŵaononge kotheratu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Ondizunza anga achite manyazi, koma musandichititse manyazi; iwo achite mantha kwambiri, koma ine mundichotsere manthawo. Tsiku la mavuto liwafikire; ndipo muwawononge kotheratu. Onani mutuwo |