Mulungu wa Israele anati, Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine; kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m'kuopa Mulungu.
Masalimo 69:6 - Buku Lopatulika Iwo akuyembekeza Inu, Ambuye, Yehova wa makamu, asachite manyazi chifukwa cha ine, iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israele, asapepulidwe chifukwa cha ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iwo akuyembekeza Inu, Ambuye Yehova wa makamu, asachite manyazi chifukwa cha ine, iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israele, asapepulidwe chifukwa cha ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, musalole kuti ndiŵachititse manyazi anthu okhulupirira Inu. Inu Mulungu wa Israele, musalole kuti anthu okufunafunani anyozeke chifukwa cha ine. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo amene amadalira Inu asanyozedwe chifukwa cha ine, Inu Ambuye Wamphamvuzonse. Iwo amene amafunafuna Inu asachititsidwe manyazi chifukwa cha ine, Inu Mulungu wa Israeli. |
Mulungu wa Israele anati, Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine; kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m'kuopa Mulungu.
Inde, onse akuyembekezera Inu sadzachita manyazi; adzachita manyazi iwo amene achita monyenga kopanda chifukwa.
Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.
Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.
Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m'menemo.
Wochokera mu mbeu yake Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israele Mpulumutsi, Yesu;
Ndipo m'mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m'dzina lanji, mwachita ichi inu?