Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 4:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo m'mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m'dzina lanji, mwachita ichi inu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo m'mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m'dzina lanji, mwachita ichi inu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono adaimiritsa Petro ndi Yohane pakati pao naŵafunsa kuti, “Kodi zija mudachitazi, mudazichita ndi mphamvu yanji, kaya mudazichita m'dzina la yani?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iwo anayimiritsa Petro ndi Yohane patsogolo pawo nayamba kuwafunsa kuti, “Kodi munachita zimenezi ndi mphamvu yanji kapena mʼdzina la yani?”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 4:7
12 Mawu Ofanana  

Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkulu ndi woweruza wathu? Kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha Mwejipito? Ndipo Mose anachita mantha, nanena, Ndithu chinthuchi chadziwika.


Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?


nanena naye, Izi muzichita ndi ulamuliro wotani? Kapena anakupatsani ndani ulamuliro uwu wakuchita izi?


Chifukwa chake Ayuda anayankha nati kwa Iye, Mutionetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi?


Koma alembi ndi Afarisi anabwera naye kwa Iye mkazi wogwidwa m'chigololo, ndipo pamene anamuimika iye pakati,


Koma iwo, m'mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.


zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.


ndi Anasi mkulu wa ansembe, ndi Kayafa, ndi Yohane, ndi Aleksandro, ndi onse amene anali a fuko la mkulu wa ansembe.


Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu,


Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa