Ngati amuna a m'hema mwanga sanati, ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?
Masalimo 57:3 - Buku Lopatulika Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adzandiyankha ali kumwamba, ndipo adzandipulumutsa. Iye adzasokoneza amene andipondereza. Adzaonetsa chikondi chake chosasinthika, adzaonetsa kukhulupirika kwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa, kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri. Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake. |
Ngati amuna a m'hema mwanga sanati, ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?
Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.
Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.
Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere; zindifikitse kuphiri lanu loyera, kumene mukhala Inuko.
Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi, nadzitukumula ngati mkango waumuna. Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira, utamwa mwazi wa zophedwa.
Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.
Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku chilingiriro chonse cha Ayuda.