Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.
Masalimo 41:1 - Buku Lopatulika Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso. |
Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.
Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo;
Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m'manja a anthu amene uwaopa.
Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.
M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.
Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.
Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.
Popeza unasunga mau a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza padziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.
Ndipo mpongozi wake ananena naye, Unakatola kuti khunkha lero? Ndi ntchito udaigwira kuti? Adalitsike iye amene anakusamalira. Ndipo anamfotokozera mpongozi wake munthu amene anakagwirako ntchito, nati, Dzina lake la munthuyo ndinakagwirako ntchito lero ndiye Bowazi.