Masalimo 26:12 - Buku Lopatulika Phazi langa liponda pachidikha, m'misonkhano ndidzalemekeza Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Phazi langa liponda pachidikha, m'masonkhano ndidzalemekeza Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndili wokhazikika pa malo opanda zovuta, ndipo ndidzatamanda Chauta pa msonkhano waukulu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndayima pa malo wopanda zovuta ndipo ndidzatamanda Yehova mu msonkhano waukulu. |
Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova; akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova.
Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, munditsogolere panjira yachidikha, chifukwa cha adani anga.
Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.
Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwachita ufumu, akulu a Yuda, ndi a upo wao, akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali.
Adzasunga mapazi a okondedwa ake, koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima; pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.