Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 68:27 - Buku Lopatulika

27 Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwachita ufumu, akulu a Yuda, ndi a upo wao, akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwachita ufumu, akulu a Yuda, ndi a upo wao, akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Patsogolo pao pali Benjamini mng'ono wa onsewo, akalonga a Yuda ali pambuyo, ndiponso akalonga a Zebuloni ndi akalonga a Nafutali.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Pali fuko lalingʼono la Benjamini, kuwatsogolera, pali gulu lalikulu la ana a mafumu a Yuda, ndiponso pali ana a mafumu a Zebuloni ndi Nafutali.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:27
17 Mawu Ofanana  

tili abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng'ono ali ndi atate wathu m'dziko la Kanani.


Ndipo Abinere analankhulanso m'kumva kwa Abenjamini; Abinere anamukanso ku Hebroni kulankhula m'makutu a Davide zonse zakukomera Aisraele ndi a nyumba yonse ya Benjamini.


Ndipo anadza ena a ana a Benjamini ndi Yuda kulinga kwa Davide.


Ndi a ana a Benjamini, abale a Saulo, zikwi zitatu; pakuti mpaka pomwepo ochuluka a iwowa anaumirira nyumba ya Saulo.


Ndipo Davide anasonkhanitsira Aisraele onse ku Yerusalemu, akwere nalo likasa la Yehova kumalo kwake adalikonzera.


Wachisanu ndi chinai wa mwezi wachisanu ndi chinai ndiye Abiyezere Mwanatoti wa Abenjamini; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.


Phazi langa liponda pachidikha, m'misonkhano ndidzalemekeza Yehova.


Akulu a anthu asonkhana akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu; akwezeka kwakukulu Iyeyo.


Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga; ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga.


Ndipo nsanje ya Efuremu idzachoka, ndi iwo amene avuta Yuda adzadulidwa; Efuremu sachitira nsanje Yuda, ndi Yuda sachitira nsanje Efuremu.


Imvani inu ichi, banja la Yakobo, amene mutchedwa ndi dzina la Israele, amene munatuluka m'madzi a Yuda amene mulumbira dzina la Yehova ndi kutchula dzina la Mulungu wa Israele, koma si m'zoona, pena m'chilungamo.


Wa fuko la Benjamini, Elidadi mwana wa Kisiloni.


Ndipo Yehova anakantha Benjamini pamaso pa Israele; ndi ana a Israele anawaononga a Benjamini tsiku lija amuna zikwi makumi awiri ndi zisanu, kudza zana limodzi; awa onse ndiwo akusolola lupanga.


Zebuloni ndiwo anthu anataya moyo wao mpaka imfa, Nafutali yemwe poponyana pamisanje.


Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling'ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa