zonsezi, mfumu, Arauna akupatsani mfumu. Ndipo Arauna anati kwa mfumu, Yehova Mulungu wanu akulandireni.
Masalimo 20:4 - Buku Lopatulika likupatse cha mtima wako, ndipo likwaniritse upo wako wonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 likupatse cha mtima wako, ndipo likwaniritse upo wako wonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akupatse zimene mtima wako ukukhumba, akuthandize kuti zonse zimene wakonza zichitikedi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akupatse chokhumba cha mtima wako ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike. |
zonsezi, mfumu, Arauna akupatsani mfumu. Ndipo Arauna anati kwa mfumu, Yehova Mulungu wanu akulandireni.
Ndipo mfumu Solomoni anampatsa mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse, chilichonse anachipempha, osawerengera zija adabwera nazo kwa mfumu. Momwemo anabwerera, namuka ku dziko lake, iyeyu ndi anyamata ake.
Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.
Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa.
Koma mkazi wake ananena naye, Yehova akadafuna kutipha, sakadalandira nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa padzanja lathu, kapena kutionetsa izi zonse, kapena kutimvetsa zoterezi nthawi ino.
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.