2 Mbiri 9:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo mfumu Solomoni anampatsa mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse, chilichonse anachipempha, osawerengera zija adabwera nazo kwa mfumu. Momwemo anabwerera, namuka ku dziko lake, iyeyu ndi anyamata ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo mfumu Solomoni anampatsa mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse, chilichonse anachipempha, osawerengera zija adabwera nazo kwa mfumu. Momwemo anabwerera, namuka ku dziko lake, iyeyu ndi anyamata ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Tsono Solomoni adapatsa mfumukazi ya ku Sheba ija zonse zimene inkafuna ndiponso chilichonse chimene idaapempha, osaŵerengera zimene anali ataipatsa kale posinthana nayo mphatso. Tsono mfumukaziyo idabwerera ku dziko lakwao pamodzi ndi atumiki ake aja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha ndipo Solomoni anayipatsa mfumuyo zoposa zimene iyo inabweretsa kwa Solomoni. Ndipo mfumuyo inabwerera ku dziko lake pamodzi ndi atumiki ake. Onani mutuwo |