Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.
Masalimo 2:11 - Buku Lopatulika Tumikirani Yehova ndi mantha, ndipo kondwerani ndi chinthenthe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tumikirani Yehova ndi mantha, ndipo kondwerani ndi chinthenthe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tumikirani Chauta mwamantha ndi monjenjemera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tumikirani Yehova mwa mantha ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera. |
Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.
Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;
Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;