Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oimbira Yehova, ndi kulemekeza chiyero chokometsetsa, pakutuluka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha.
Masalimo 18:4 - Buku Lopatulika Zingwe za imfa zinandizinga, ndipo mitsinje ya zopanda pake inandiopsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zingwe za imfa zinandizinga, ndipo mitsinje ya zopanda pake inandiopsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthambo za imfa zidandizungulira, mitsinje yothamanga yoononga idandisefukira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zingwe za imfa zinandizinga; mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri. |
Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oimbira Yehova, ndi kulemekeza chiyero chokometsetsa, pakutuluka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha.
Ndipo poyamba iwo kuimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amowabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.
Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.
Pakuti andizinga agalu, msonkhano wa oipa wanditsekereza; andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.
ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.
Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu.
Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mu Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwire.
Ndipo mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa mu Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa.
koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;