Masalimo 12:5 - Buku Lopatulika Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chifukwa choti osauka alandidwa zao ndipo osoŵa akudandaula, Chauta akunena kuti, “Ndichitapo kanthu tsopano, ndiŵapulumutsa monga momwe akufuniramo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu ndi kubuwula kwa anthu osowa, Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova, “Ndidzawateteza kwa owazunza.” |
kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa.
Mayendedwe ake alimbika nthawi zonse; maweruzo anu ali pamwamba posaona iye; adani ake onse awanyodola.
Ha! Kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu, kumene munachitira iwo akukhulupirira Inu, pamaso pa ana a anthu!
Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.
Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israele apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israele apite.
Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.
Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.
Ndipo chidzakhala chizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Ejipito; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, chifukwa cha osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.
Atate wake, popeza anazunza chizunzire, nafunkha za mbale wake, nachita chimene sichili chabwino pakati pa anthu ake, taona, adzafa mu mphulupulu yake.
Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa chipongwe cha lilime lao; ichi ndicho adzawasekera m'dziko la Ejipito.
Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.
Pamenepo anachotsa milungu yachilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israele.