Chifukwa chake ndinawaika potera m'kati mwa linga, popenyeka; inde ndinaika anthu monga mwa mabanja ao, akhale nao malupanga ao, nthungo zao, ndi mauta ao.
Masalimo 112:5 - Buku Lopatulika Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu amene amakongoza mosafuna phindu, amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu, amene amachita ntchito yake mwachilungamo. |
Chifukwa chake ndinawaika potera m'kati mwa linga, popenyeka; inde ndinaika anthu monga mwa mabanja ao, akhale nao malupanga ao, nthungo zao, ndi mauta ao.
Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.
Ndipo taonani, munthu dzina lake Yosefe, ndiye mkulu wa milandu, munthu wabwino ndi wolungama
Koma takondanani nao adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.
Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.
chifukwa anali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro: ndipo khamu lalikulu lidaonjezeka kwa Ambuye.
Pakuti ndi chivuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino.
Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chionjezere, m'chidziwitso, ndi kuzindikira konse;