Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 6:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Anthu onsewo atakhuta, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Tolani zotsala kuti pasatayikepo kanthu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, “Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 6:12
12 Mawu Ofanana  

Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.


Ndipo analanda mizinda yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zaozao nyumba zodzala ndi zokoma zilizonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda ya azitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukulu.


Wogwira ntchito mwaulesi ndiye mbale wake wa wosakaza.


Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, ndipo eni chuma anawachotsa opanda kanthu.


Ndipo pakupita masiku owerengeka mwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko.


Ndipo Iye ananenanso kwa ophunzira ake, Panali munthu mwini chuma, anali ndi kapitao wake; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza chuma chake.


Ndipo anadya, nakhuta onsewo; natola makombo, madengu khumi ndi awiri.


Ndipo Yesu yemwe ndi ophunzira ake anaitanidwa kuukwatiwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa