Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.
Masalimo 112:2 - Buku Lopatulika Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mbeu yake idzakhala yamphamvu pa dziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko; mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa. |
Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.
Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isaki mwana wake; ndipo Isaki anakhala pa Beere-Lahai-Roi.
Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino; koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake.
ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;
Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.