Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 7:62 - Buku Lopatulika

62 chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

62 chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

62 Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

62 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani;

Onani mutuwo Koperani




Numeri 7:62
11 Mawu Ofanana  

Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.


Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magaleta, ndi m'machila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamira, kudza kuphiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israele abwera nazo nsembe zao m'chotengera chokonzeka kunyumba ya Yehova.


Ndipo iye adzapangana chipangano cholimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.


chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;


ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;


kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.


Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.


Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.


Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.


Ndipo anadza mngelo wina, naima paguwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse paguwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu.


Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kutuluka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa