Masalimo 102:5 - Buku Lopatulika Chifukwa cha liu la kubuula kwanga mnofu wanga umamatika kumafupa anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa cha liu la kubuula kwanga mnofu wanga umamatika kumafupa anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndaonderatu ngati munthu wachitopa, ntchito yanga ndi kubuula nthaŵi zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa cha kubuwula kwanga kofuwula ndatsala chikopa ndi mafupa okhaokha. |
Fupa langa laumirira pa khungu langa ndi mnofu wanga, ndipo ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga.
Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.
Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake; pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga.
Maonekedwe ao ada koposa makala, sazindikirika m'makwalala; khungu lao limamatira pa mafupa ao, lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.
Ndipo popeza munthuyo adatero chaka ndi chaka, popita mkaziyo kunyumba ya Yehova, mnzakeyo amamputa; chifukwa chake iye analira misozi, nakana kudya.