Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 1:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo popeza munthuyo adatero chaka ndi chaka, popita mkaziyo kunyumba ya Yehova, mnzakeyo amamputa; chifukwa chake iye analira misozi, nakana kudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo popeza munthuyo adatero chaka ndi chaka, popita mkaziyo kunyumba ya Yehova, mnzakeyo amamputa; chifukwa chake iye analira misozi, nakana kudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Zimenezi zinkachitika chaka ndi chaka. Nthaŵi zonse akamapita ku nyumba ya Chauta, mkazi mnzakeyo ankamputa. Nchifukwa chake Hana ankangolira, ndipo sankafuna ndi kudya komwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Izi zimachitika chaka ndi chaka. Hana ankati akamapita ku Nyumba ya Yehova mkazi mnzakeyo ankamunyogodola. Choncho Hana ankangokhalira kulira osafuna ndi kudya komwe.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 1:7
7 Mawu Ofanana  

Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota; popeza ndiiwala kudya mkate wanga.


Chifukwa cha liu la kubuula kwanga mnofu wanga umamatika kumafupa anga.


anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang'amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndi lubani m'manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.


Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukulu, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yake.


Ndipo mwamuna wake Elikana anati kwa iye, Hana, umaliriranji? Ndipo umakaniranji kudya? Ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindili wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?


Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu.


Ndiponso amake akamsokera mwinjiro waung'ono, nabwera nao kwa iye chaka ndi chaka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wake kudzapereka nsembe ya pachaka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa