Masalimo 102:3 - Buku Lopatulika Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi, ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi, ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Masiku anga amangopita ngati utsi, ndipo thupi langa likuyaka ngati ng'anjo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti masiku anga akupita ngati utsi; mafupa anga akunyeka ngati nkhuni zoyaka. |
Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.
Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo. Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.
Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa; ndipo chifukwa cha dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.
Pakuti oipa adzatayika, ndipo adani ake a Yehova adzanga mafuta a anaankhosa; adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.
Mumnofu mwanga mulibe chamoyo chifukwa cha ukali wanu; ndipo m'mafupa anga simuzizira, chifukwa cha cholakwa changa.
Anatumiza moto wochokera kumwamba kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa; watchera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo; wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.
inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.