Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 102:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pakuti masiku anga akupita ngati utsi; mafupa anga akunyeka ngati nkhuni zoyaka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi, ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi, ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Masiku anga amangopita ngati utsi, ndipo thupi langa likuyaka ngati ng'anjo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 102:3
11 Mawu Ofanana  

Khungu langa layamba kuda ndipo likufunduka; thupi langa likutentha chifukwa cha kuphwanya kwa thupi.


Ngakhale ndili ngati thumba lachikopa la vinyo pa utsi sindiyiwala zophunzitsa zanu.


Musandibisire nkhope yanu, musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo; mwakhala muli thandizo langa. Musandikane kapena kunditaya, Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.


Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula; mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso, ndipo mafupa anga akulefuka.


Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa, chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.


Koma oyipa adzawonongeka; adani a Yehova adzakhala ngati kukongola kwa kuthengo, iwo adzazimirira ngati utsi.


Chifukwa cha ukali wanu mulibe thanzi mʼthupi langa; mafupa anga alibe mphamvu chifukwa cha tchimo langa.


“Anatumiza moto kuchokera kumwamba, unalowa mpaka mʼmafupa anga. Anayala ukonde kuti ukole mapazi anga ndipo anandibweza. Anandisiya wopanda chilichonse, wolefuka tsiku lonse.


Wakalambitsa khungu langa ndi mnofu wanga, ndipo waphwanya mafupa anga.


Chifukwa chiyani mukutero? Inu simukudziwa zimene ziti zichitike mawa. Kodi moyo wanu ndi wotani? Inu muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa ndipo kenaka ndikuzimirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa