Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 1:13 - Buku Lopatulika

13 Anatumiza moto wochokera kumwamba kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa; watchera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo; wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Anatumiza moto wochokera kumwamba kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa; watchera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo; wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Adatumiza moto kuchokera Kumwamba. Udaloŵa mpaka m'kati mwa mafupa anga. Adayala ukonde kuti akole mapazi anga, nandibweza. Adandisiya ndili ndi chisoni chachikulu, ndili wolefuka tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 “Anatumiza moto kuchokera kumwamba, unalowa mpaka mʼmafupa anga. Anayala ukonde kuti ukole mapazi anga ndipo anandibweza. Anandisiya wopanda chilichonse, wolefuka tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 1:13
31 Mawu Ofanana  

Pakuti aponyedwa mu ukonde ndi mapazi ake, namaponda pamatanda.


Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga, nandizinga ndi ukonde wake.


Khungu langa lada, nilindifundukira; ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao.


Achite manyazi nabwerere m'mbuyo. Onse akudana naye Ziyoni.


Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.


Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.


Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo. Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.


Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga; abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.


Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa, ndabangula chifukwa cha kumyuka mtima wanga.


Munapita nafe kuukonde; munatisenza chothodwetsa pamsana pathu.


Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ai, koma yoocha pamoto; mutu wake ndi miyendo yake ndi matumbo ake.


Iwo adzabwezedwa m'mbuyo, adzakhala ndi manyazi ambiri amene akhulupirira mafano osemedwa, nati kwa mafano oyengeka, Inu ndinu milungu yathu.


Chifukwa chake mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m'mizinda ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe.


Zoipa zao zonse zidze pamaso panu, muwachitire monga mwandichitira ine chifukwa cha zolakwa zanga zonse, pakuti ndiusa moyo kwambiri, ndi kulefuka mtima wanga.


Wapambutsa njira zanga, nanding'amba; nandipululutsa.


Chifukwa cha ichi mtima wathu ufooka, chifukwa cha izi maso athu achita chimbuuzi;


Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babiloni, ku dziko la Ababiloni; sadzaliona, chinkana adzafako.


Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babiloni, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwake anandilakwira nako.


Atero Ambuye Yehova, Ndidzakuponyera khoka langa mwa msonkhano wa mitundu yambiri ya anthu, nadzakuvuulira m'khoka mwanga.


Pamene amuka ndidzawayalira ukonde wanga, ndidzawagwetsa ngati mbalame za m'mlengalenga, ndidzawalanga monga udamva msonkhano wao.


Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.


Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamau, m'mafupa mwanga mudalowa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.


Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.


m'lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu;


Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa