Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?
Masalimo 10:6 - Buku Lopatulika Ati mumtima mwake, Sindidzagwedezeka ine; ku mibadwomibadwo osagwa m'tsoka ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ati mumtima mwake, Sindidzagwedezeka ine; ku mibadwomibadwo osagwa m'tsoka ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumtima mwake amaganiza kuti, “Sindidzagwedezeka, sindidzaona konse mavuto.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye amadziyankhulira kuti, “Palibe chimene chidzandigwedeze. Ndidzakhala wokondwa nthawi zonse ndipo sindidzakhala pa mavuto.” |
Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?
Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.
Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.
Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.
Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalire izi mumtima mwako, kapena kukumbukira chomalizira chake.
Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta chakumwa chaukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikulu loposa ndithu.
Pakuti chinkana akunga minga yoyangayanga, naledzera nacho choledzeretsa chao, adzathedwa konse ngati chiputu chouma.
Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.
Monga momwe unadzichitira ulemu, nudyerera, momwemo muuchitire chouzunza ndi chouliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.