amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao;
Marko 5:2 - Buku Lopatulika Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu atangotuluka m'chombo, munthu wina wogwidwa ndi mzimu woipa adadzakumana naye kuchokera ku manda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atatuluka mʼbwato, munthu amene anali ndi mzimu woyipa anachoka ku manda ndi kukumana naye. |
amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao;
Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anafuula iye.
Ndipo anati kwa ophunzira ake, kuti kangalawa kamlinde Iye, chifukwa cha khamulo, kuti angamkanikize Iye,
Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja.
Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye.
Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja.
amene anayesa nyumba yake kumanda; ndipo palibe munthu anakhoza kummanganso, inde ngakhale ndi unyolo;
Koma pomwepo mkazi, kabuthu kake kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake.
Ndipo atatuluka pamtunda Iye, anakomana naye mwamuna wa kumzinda, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanavale chovala, nisanakhala m'nyumba, koma m'manda.
Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake.