Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 1:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kufuula ndi mau aakulu, unatuluka mwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kufuula ndi mau akulu, unatuluka mwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Apo mzimu womuipitsa uja udamugwedeza kwamphamvu munthuyo, ndipo udakuwa koopsa, nkutuluka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Mzimu woyipawo unamugwedeza mwamphamvu ndipo unatuluka mwa iye ukufuwula.

Onani mutuwo Koperani




Marko 1:26
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli chete, nutuluke mwa iye.


Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye.


Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng'amba koopsa; ndipo anagwa pansi navimvinika ndi kuchita thovu.


Ndipo pamene unafuula, numng'ambitsa, unatuluka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira.


koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamgonjetsa, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake.


ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, suchoka pa iye, koma umsautsa koopsa.


Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa