Marko 4:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Yesu adayambanso kuphunzitsa pambali pa Nyanja ya Galileya. Anthu ochuluka adasonkhana kumeneko, kotero kuti Iye adaayenera kuloŵa m'chombo, nakhala pansi m'menemo panyanjapo. Anthu onse adaakhala pansi pa mtunda m'mphepete mwa nyanjayo, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Nthawi inanso Yesu atakhala mʼmbali mwa nyanja, anayamba kuphunzitsa. Gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira kotero kuti Iye analowa mʼbwato lomwe linali pa nyanja nakhalamo, anthu onse ali pa mtunda mʼmbali mwa madzi. Onani mutuwo |