Marko 4:2 - Buku Lopatulika Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri m'mafanizo, nanena nao m'chiphunzitso chake, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri m'mafanizo, nanena nao m'chiphunzitso chake, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo Yesu adayamba kuŵaphunzitsa zambiri m'mafanizo. Poŵaphunzitsa adati, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anawaphunzitsa zinthu zambiri mʼmafanizo, ndipo mʼchiphunzitso chake anati: |
Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Chifukwa chanji muphiphiritsira iwo m'mafanizo?
Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.
Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake:
Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordani; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso.
Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wampesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.
Ndipo m'chiphunzitso chake ananena, Yang'anirani mupewe alembi, akufuna kuyendayenda ovala miinjiro, ndi kulonjeredwa pamisika,
Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana?
Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zichitidwa m'mafanizo;