Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Yesu adalankhula nawo zambiri m'mafanizo. Adati, “Munthu wina adaapita kukafesa mbeu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pamenepo Iye anawawuza zinthu zambiri mʼmafanizo ndi kuti, “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:3
27 Mawu Ofanana  

Ndidzatchera khutu kufanizo, ndidzafotokozera chophiphiritsa changa poimbira.


Ndidzatsegula pakamwa panga mofanizira; ndidzatchula zinsinsi zoyambira kale.


Wobadwa ndi munthu iwe, ipha mwambi, nunene fanizo kwa nyumba ya Israele,


Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Anandinena, Wonena mafanizo uyu.


Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu.


Kodi sadzamnenera fanizo onsewo, ndi mwambi womnyodola, ndi kuti, Tsoka iye wochulukitsa zimene sizili zake? Mpaka liti? Iye wodzisenzera zigwiriro.


Ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nkulusira izo.


Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anachokera kumeneko.


Ndipo Yesu anayankha, nalankhulanso kwa iwo m'mafanizo, nati,


Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira;


Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wampesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.


Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nachoka.


Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana?


Ndipo ananena nao, Simudziwa kodi fanizo ili? Mukazindikira bwanji mafanizo onse?


Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, monga anakhoza kumva;


Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse?


Ndipo Iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse.


Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa