Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.
Luka 8:9 - Buku Lopatulika Ndipo ophunzira ake anamfunsa Iye, kuti, Fanizo ili lili lotani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ophunzira ake anamfunsa Iye, kuti, Fanizo ili lili lotani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzira a Yesu adamufunsa za tanthauzo la fanizoli. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzira ake anamufunsa tanthauzo lake la fanizolo. |
Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.
Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Chifukwa chanji muphiphiritsira iwo m'mafanizo?
Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.
Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo.
ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ake.
Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.