Luka 8:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo Iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo Iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Tsono Iye adati, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wake. Koma enaŵa amazimvera m'mafanizo chabe, kuti choncho ayang'ane, koma asapenye, ndipo amve, koma asamvetse.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Iye anati, “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti, “ngakhale akuona, asapenye; ngakhale akumva, asazindikire.” Onani mutuwo |