Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 8:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo zina zinagwa pa nthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso zamakumikhumi. Pakunena Iye izi anafuula, Iye amene ali ndi makutu akumva amve.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo zina zinagwa pa nthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso zamakumikhumi. Pakunena Iye izi anafuula, Iye amene ali ndi makutu akumva amve.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino. Zidakula nkubereka. Ngala iliyonse inali ndi njere makumi khumi.” Tsono Yesu adalankhula mokweza mau kuti, “Amene ali ndi makutu akumva, amve!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mbewu zina zinagwera pa nthaka yabwino. Zinamera ndipo zinabala mowirikiza 100 kuposa zimene zinafesedwa zija.” Atanena izi, anafuwula kuti, “Amene ali ndi makutu, amve.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:8
25 Mawu Ofanana  

Ndipo Isaki anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi chaka chimenecho; ndipo Yehova anamdalitsa iye.


Khutu lakumva, ndi diso lopenya, Yehova anapanga onse awiriwo.


Kodi nzeru siitana, luntha ndi kukweza mau ake?


Tamvani inu, Tcherani khutu; musanyade, pakuti Yehova wanena.


Ndipo Yehova watuma kwa inu atumiki ake onse ndiwo aneneri, pouka mamawa ndi kuwatuma; koma simunamvere, simunatchere khutu lanu kuti mumve;


Amene ali ndi makutu akumva, amve.


Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.


Ndipo iwo ofesedwa pa nthaka yabwino ndiwo oterewa akumva mau, nawalandira, nabala zipatso zakupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.


Ngati munthu ali nao makutu akumva, amve.


Ndipo zina zinagwa m'nthaka yabwino, ndipo zinapatsa zipatso, ndi kukula ndi kuchuluka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.


Suyenera kuuthira pamunda kapena padzala, autaya kunja. Amene ali nao makutu akumva amve.


Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.


Ndipo zina zinagwa pakati pa minga; ndi mingayo inaphuka pamodzi nazo, nkuzitsamwitsa.


Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.


kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;


Ngati wina ali nalo khutu, amve.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene apambana sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa