Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:36 - Buku Lopatulika

36 Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Pambuyo pake Yesu adaŵasiya anthu ambirimbiri aja, nakaloŵa m'nyumba. Tsono ophunzira ake adadzampempha kuti, “Tatimasulirani fanizo la namsongole wam'munda lija.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Kenaka Iye anasiya gulu la anthu ndi kukalowa mʼnyumba. Ophunzira ake anapita kwa Iye nati, “Timasulireni fanizo la namsongole mʼmunda.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:36
13 Mawu Ofanana  

Tsiku lomwelo Yesu anatuluka m'nyumbamo, nakhala pansi m'mbali mwa nyanja.


Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.


Ndipo tsono mverani inu fanizolo la wofesa mbeu uja.


koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo.


Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye kutsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke.


Ndipo m'mene Iye anauza makamuwo amuke, analowa m'ngalawa, nafika m'malire a Magadani.


Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.


ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ake.


Ndipo pomwepo Iye anakakamiza ophunzira ake alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m'mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke.


Ndipo m'mene Iye adalowa m'nyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ake anamfunsa Iye fanizolo.


Ndipo iwo anali ngati zikwi zinai; ndipo Iye analawirana nao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa