Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:37 - Buku Lopatulika

37 Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiye Mwana wa Munthu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiye Mwana wa Munthu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Yesu adati, “Wofesa mbeu zabwino uja ndi Mwana wa Munthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Iye anayankha nati, “Munthu amene anafesa mbewu yabwino ndi Mwana wa Munthu.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:37
16 Mawu Ofanana  

Tirigu wa mkate aperedwa; pakuti samampuntha osaleka; ngakhale kuyendetsapo njinga ya galeta wake, ngakhale kumphwanya ndi ziboda za akavalo ake sapera.


Iye wakulandira inu, andilandira Ine, ndi wakundilandira Ine, amlandira Iye amene ananditumiza Ine.


Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake;


Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafese mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo?


Ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nkulusira izo.


Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,


Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.


Iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana Iye amene anandituma Ine.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira aliyense amene ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine.


Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.


Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.


Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito,


Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana,


tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa