Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.
Luka 5:12 - Buku Lopatulika Ndipo panali, pamene Iye anali mumzinda wina, taona, munthu wodzala ndi khate; ndipo pamene anaona Yesu, anagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali, pamene Iye anali m'mudzi wina, taona, munthu wodzala ndi khate; ndipo pamene anaona Yesu, anagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yesu anali m'mudzi wina, kudabwera munthu wina wa khate thupi lonse. Pamene adaona Yesu, adadzigwetsa moŵerama pansi pamaso pake nayamba kumdandaulira. Adati, “Ambuye, mutafuna, mungathe kundichiritsa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu ali ku mudzi wina, munthu amene anali ndi khate thupi lonse anabwera kwa Iye. Munthuyo ataona Yesu, anagwa chafufumimba ndipo anamupempha Iye kuti, “Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.” |
Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.
Ndipo anthu onse anaona, nagwa nkhope zao pansi, nati, Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.
Ndipo Naamani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyake, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate.
Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbuu ngati chipale chofewa.
Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?
Ndipo Davide anakweza maso ake, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati padziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lake, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akulu ovala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.
Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.
Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lake pachifuwa pake, nalitulutsa, taonani, dzanja lake linali lakhate, lotuwa ngati chipale chofewa.
Ndipo unatuluka moto pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta paguwa la nsembe; ndipo pakuchiona anthu onse anafuula, nagwa nkhope zao pansi.
Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.
nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalinkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulumuke, ndi kukhala ndi moyo.
ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo.
Ndipo Iye anatambalitsa dzanja lake, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate linachoka kwa iye.
Chenjerani nayo nthenda yakhate, kusamaliratu, ndi kuchita monga mwa zonse akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinalamulira iwo, momwemo muzisamalira kuchita.
kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.
Nati, Iai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yake pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wake?