Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 9:28 - Buku Lopatulika

28 Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Yesu ataloŵa m'nyumba, akhungu aja adadzampeza, Iye nkuŵafunsa kuti, “Kodi mukukhulupirira kuti ndingathe kuchita zimenezi?” Iwo adati, “Inde, Ambuye.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Atalowa mʼnyumba, amuna awiri osaonawo anabwera kwa Iye ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukhulupirira kuti ndikhoza kukuchiritsani?” Iwo anayankha kuti, “Inde Ambuye.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 9:28
14 Mawu Ofanana  

Mbiya ya ufa siidathe, ndi nsupa ya mafuta siinachepe, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya.


Tsiku lomwelo Yesu anatuluka m'nyumbamo, nakhala pansi m'mbali mwa nyanja.


Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.


Ndipo Iye, chifukwa cha kusakhulupirira kwao, sanachite kumeneko zamphamvu zambiri.


Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo.


Ndipo onani, wakhate anadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.


Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo.


Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.


Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Chichitidwe kwa inu monga chikhulupiriro chanu.


ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?


Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?


Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi chikhulupiriro cholandira nacho moyo,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa