Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 9:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Pamene Yesu ankachoka kumeneko, anthu aŵiri akhungu adamtsatira. Ankafuula kuti, “Inu Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Yesu atapitirira ulendo wake, amuna awiri osaona anamutsatira Iye, akufuwula kuti, “Tichitireni chifundo, Mwana wa Davide!”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 9:27
24 Mawu Ofanana  

Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.


akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.


Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.


Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi.


Ndipo pamene iwo analikutuluka mu Yeriko, khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye.


Koma ansembe aakulu ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,


Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!


Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.


Wolemekezeka Ufumu ulinkudza, wa atate wathu Davide; Hosana mu Kumwambamwamba.


Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo.


ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, mutichitire chifundo.


Koma Iye anati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Khristuyo ndiye mwana wa Davide?


Nthawi yomweyo Iye anachiritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zovuta, ndi ziwanda; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.


Kodi sichinati chilembo kuti Khristu adza kutuluka mwa mbeu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide?


wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi,


a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa