Genesis 18:14 - Buku Lopatulika14 Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Kodi pali chimene chikhoza kumukanika Yehova? Pa nthawi yake, ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzabala mwana wamwamuna.” Onani mutuwo |
Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, ndipo zifa ndi ludzu.