Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 7:3 - Buku Lopatulika

3 Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Nthaŵi imeneyo panali anthu akhate anai amene ankakhala pa chipata. Iwowo adayamba kufunsana kuti, “Chifukwa chiyani tikungotambalala pano kumangodikira imfa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsono pa chipata cholowera mu mzinda wa Samariya pankakhala anthu anayi akhate. Iwo anayankhulana kuti, “Chifukwa chiyani tikungokhala pano kudikira kufa?

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 7:3
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Naamani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyake, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate.


Tikati, Tilowe m'mzinda, m'mzinda muli njala, tidzafa m'mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa.


Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikulu zonse Elisa wazichita.


Mudzaferanji, iwe ndi anthu anu, ndi lupanga ndi njala, ndi mliri, monga wanena Yehova za mtundu umene ukana kumtumikira mfumu ya ku Babiloni?


Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'mizinda yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova.


Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbuu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wake akadamlavulira malovu pankhope pake sakadachita manyazi masiku asanu ndi awiri? Ambindikiritse kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa