2 Mafumu 7:4 - Buku Lopatulika4 Tikati, Tilowe m'mzinda, m'mzinda muli njala, tidzafa m'mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Tikati, Tilowe m'mudzi, m'mudzi muli njala, tidzafa m'mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Tikati tiyeni tiloŵe mumzindamu, njala ili m'menemo kumene, ndiye tikaferamo. Komanso tikangotambalala pompano, tifabe. Tsono tiyeni tingopita ku zithando za Asiriya. Akatileka ndi moyo, chabwino, koma akatipha, palibe kanthu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Ngati tinganene kuti, ‘Tidzalowa mu mzinda,’ njala ili mu mzindamo ndipo tidzafa. Ndipo ngati tikhalebe pano, tidzafa ndithu. Choncho tiyeni tipite ku msasa wa Aaramu ndi kukadzipereka. Ngati sakatipha, tidzakhala ndi moyo, ngati akatipha, basi tikafa.” Onani mutuwo |