2 Mafumu 7:2 - Buku Lopatulika2 Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira padzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira pa dzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Tsono phungu wokhulupirika wa mfumu adafunsa munthu wa Mulungu uja kuti, “Ngakhale Chauta mwiniwake atachita kutikhuthulira mvula yochuluka chotani, zoterezi nkuchitika ngati?” Koma Elisa adati, “Ndithu udzaziwona zimenezo ndi maso ako, koma iweyo sudzazilaŵa.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Mtsogoleri amene mfumu inkamudalira anati kwa munthu wa Mulungu, “Taona, ngakhale Yehova atatsekula zipata zakumwamba, kodi zimenezi zingachitikedi?” Elisa anamuyankha kuti, “Taona, iweyo udzaziona zimenezi ndi maso ako, koma sudzadyako kanthu.” Onani mutuwo |