2 Mafumu 5:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Naamani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyake, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Naamani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyake, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Panali mkulu wina wa gulu lankhondo la mfumu ya ku Siriya, dzina lake Naamani, amene anali munthu wokhulupirika kwambiri kwa mbuye wake. Mbuye wakeyo ankamkonda Naamaniyo kwambiri, chifukwa choti ankhondo ake ankapambana pa nkhondo, popeza kuti Chauta anali naye Naamaniyo. Naamaniyo anali munthu wamphamvu ndiponso wolimba mtima, koma anali wakhate. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Tsono Naamani anali mtsogoleri wa gulu lankhondo a mfumu ya ku Aramu. Iye anali munthu wodalirika pamaso pa mbuye wake ndipo anali wokondedwa kwambiri, chifukwa kudzera mwa iye Yehova anapambanitsa Aaramu. Anali msilikali wolimba mtima, koma anali ndi khate. Onani mutuwo |