Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 5:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Aaramu adatuluka magulumagulu, nabwera nalo m'ndende buthu lochokera ku dziko la Israele, natumikira mkazi wa Naamani iyeyu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Aaramu adatuluka magulumagulu, nabwera nalo m'ndende buthu lochokera ku dziko la Israele, natumikira mkazi wa Naamani iyeyu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Nthaŵi ina Asiriya adaagwirako mtsikana ku dziko la Israele kumene adakathirako nkhondo, ndipo mtsikanayo adasanduka mdzakazi wa mkazi wa Naamani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Tsono magulu a Aaramu anapita ku nkhondo ndipo anakagwira ukapolo mtsikana wamngʼono wa ku Israeli, ndipo ankatumikira mkazi wa Naamani.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 5:2
6 Mawu Ofanana  

Pamenepo Elisa anamwalira, ndipo anamuika. Ndipo magulu a Amowabu analowa m'dziko poyambira chaka.


Nati uyu kwa mbuyake wamkazi, Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali mu Samariya, akadamchiritsa khate lake.


Ndipo anawakonzera chakudya chambiri, nadya namwa iwo; nawauza amuke; namuka kwa mbuye wao. Ndipo magulu a Aramu sanadzenso ku dziko la Israele.


Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la ambuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo.


Pamenepo Abimeleki anauka ndi anthu onse anali naye, usiku; nalalira a ku Sekemu, magulu anai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa