Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 5:3 - Buku Lopatulika

3 Nati uyu kwa mbuyake wamkazi, Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali mu Samariya, akadamchiritsa khate lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nati uyu kwa mbuyake wamkazi, Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m'Samariya, akadamchiritsa khate lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono mtsikana uja adauza mkazi wa Naamani kuti, “Bwanji kodi osati ambuyanga apite kwa mneneri ku Samariya, kuti mneneriyo akaŵachize khate laoli.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mtsikanayo anawuza mkazi wa Naamani kuti, “Mbuye wanga akanapita kukaonana ndi mneneri amene amakhala ku Samariya, akanachiritsidwa khate lawo.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 5:3
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Aaramu adatuluka magulumagulu, nabwera nalo m'ndende buthu lochokera ku dziko la Israele, natumikira mkazi wa Naamani iyeyu.


Ndipo analowa wina, nauza mbuye wake, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israele lanena zakutizakuti.


Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israele adang'amba zovala zake, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zovala zanu chifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israele.


Koma Mose anati kwa iye, Kodi uchita nsanje nao chifukwa cha ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri? Mwenzi Yehova atawaikira mzimu wake!


akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.


Ndipo Paulo anati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang'ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndili ine, osanena nsinga izi.


Mwadzala kale, mwalemerera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa