m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.
Genesis 5:5 - Buku Lopatulika Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adamwalira ali wa zaka 930. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira. |
m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.
Masiku ake Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi.
masiku ake onse a Seti anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi ndi ziwiri; ndipo anamwalira.
Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sangathe kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye.
Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa? Amene adzapulumutsa moyo wake kumphamvu ya manda?
Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.
inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; katungurume adzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;
fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.
Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.
Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.
kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.