Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 3:19 - Buku Lopatulika

19 m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Udzayenera kukhetsa thukuta kuti upeze chakudya, mpaka udzabwerera kunthaka komwe udachokera. Udachokera ku dothi, udzabwereranso kudothi komweko.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Kuti upeze chakudya udzayenera kukhetsa thukuta, mpaka utabwerera ku nthaka pakuti unachokera kumeneko; pakuti ndiwe fumbi ku fumbi komweko udzabwerera.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 3:19
33 Mawu Ofanana  

Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa:


Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.


Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.


minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m'thengo:


Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira.


nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.


Mukumbukire kuti mwandiumba ngati dothi; ndipo kodi mudzandibwezera kufumbi?


Ndipo khungu langa litaonongeka, pamenepo wopanda thupi langa, ndidzapenya Mulungu,


Iwo agona chimodzimodzi kufumbi, ndi mphutsi ziwakuta.


zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi, ndi munthu adzabwerera kufumbi.


kopambana kotani nanga iwo akukhala m'nyumba zadothi, amene kuzika kwao kuli m'fumbi, angothudzulidwa ngati njenjete.


Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.


Pamenepo munthu atulukira kuntchito yake, nagwiritsa kufikira madzulo.


Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa; mukalanda mpweya wao, zikufa, ndipo zibwerera kufumbi kwao.


Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.


Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.


Onenepa onse a padziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.


Mubweza munthu akhale fumbi; nimuti, Bwererani inu, ana a anthu.


Munthu wosochera panjira ya nzeru adzakhala m'msonkhano wa akufa.


Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo; ntchito yovuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.


Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zimpindulira chiyani?


fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.


Onse apita kumalo amodzi; onse achokera m'fumbi ndi onse abweranso kufumbi.


Monga anatuluka m'mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m'dzanja lake.


Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha.


Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba.


Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.


Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chivuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.


Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ichi, Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.


Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa