Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 3:18 - Buku Lopatulika

18 minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m'thengo:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m'thengo:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 M'nthakamo mudzamera zitsamba za minga ndi za nthula, ndipo iwe udzadya zomera zakuthengo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Mʼnthakamo mudzamera minga ndi nthula ndipo udzadya zomera zakuthengo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 3:18
20 Mawu Ofanana  

Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako:


m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.


nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.


imere minga m'malo mwa tirigu, ndi dawi m'malo mwa barele. Mau a Yobu atha.


Zokolola zao anjala azidya, azitenga ngakhale kuminga, ndi aludzu ameza chuma chao.


muvala ulemu ndi chifumu. Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala; ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga.


Mubweza munthu akhale fumbi; nimuti, Bwererani inu, ana a anthu.


Minga ndi misampha ili m'njira ya wokhota; koma wosunga moyo wake adzatalikira imeneyo.


Taonani, ponsepo panamera minga, ndi kuwirirapo khwisa; tchinga lake lamiyala ndi kupasuka.


Padziko la anthu anga padzafika minga ndi lunguzi; inde pa nyumba zonse zokondwa, m'mzinda wokondwerera;


ndipo ndidzaupasula; sudzadzomboleredwa kapena kulimidwa; koma padzamera lunguzi ndi minga; ndidzalamuliranso mitambo kuti isavumbwepo mvula.


Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti paliponse panali mipesa chikwi chimodzi ya mtengo wake wa sekeli chikwi chimodzi, padzakhala lunguzi ndi minga.


Munthu adzafikako ndi mivi ndi uta; pakuti dziko lonse lidzakhala la lunguzi ndi minga.


Abzala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.


Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga.


Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nkuzitsamwitsa izo.


Munthu mmodzi akhulupirira kuti adye zinthu zonse, koma wina wofooka angodya zitsamba.


koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.


dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa