Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 3:17 - Buku Lopatulika

17 Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Kenaka Mulungu adauza Adamu kuti, “Iwe unamvera mkazi wako, wadya zipatso zija zimene ndidaakuuza kuti usadye. Nthaka idzatembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi. Udzayenera kugwira ntchito yathukuta nthaŵi ya moyo wako wonse, kuti upeze chakudya chokwanira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’ “Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe, movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo masiku onse a moyo wako.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 3:17
28 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamaliseche? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye?


minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m'thengo:


Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wopatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene anali naye, nadya iyenso.


namutcha dzina lake Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pantchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova;


Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.


Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.


Ngati nyali za oipa zizimidwa kawirikawiri? Ngati tsoka lao liwagwera? Ngati Mulungu awagawira zowawa mu mkwiyo wake?


Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.


Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.


Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Inde masiku ake onse amadya mumdima, ndipo zimchulukira chisoni ndi nthenda ndi mkwiyo.


nanena kwa iye, Mnzangawe, unalowa muno bwanji wosakhala nacho chovala cha ukwati? Ndipo iye analibe mau.


Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundichitira ichi Ine.


Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiike, ndi wotuta chimene sindinachifese;


Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa