Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 48:18 - Buku Lopatulika

Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pamutu wake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pa mutu wake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adauza bambo wake kuti, “Musatero atate. Wamkulu ndi uyu. Dzanja lanu lamanja likhale pamutu pa ameneyu.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

nati kwa abambo ake, “Ayi, abambo anga, uyu ndiye woyamba kubadwa, ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.”

Onani mutuwo



Genesis 48:18
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Loti anati kwa iwo, Iaitu, mfumu;


Ndipo Rebeka anatenga zovala zokoma za Esau mwana wake wamkulu zinali m'nyumba, naveka nazo Yakobo mwana wake wamng'ono;


Ndipo Labani anati, Satero kwathu kuno, kupatsa wamng'ono asanapatse wamkulu.


Ndipo anakhala pamaso pake, woyamba monga ukulu wake, ndi wamng'ono monga ung'ono wake; ndipo anazizwa wina ndi wina.


Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wake anaika dzanja lake lamanja pamutu wa Efuremu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wake, kulichotsa pamutu wa Efuremu ndi kuliika pamutu wa Manase.


Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri.


Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga; ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.


Chotero ai, mukani tsopano, inu amuna aakulu, tumikirani Yehova pakuti ichi muchifuna. Ndipo anawapirikitsa pamaso pa Farao.


Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.


Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadye ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.


Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse.