Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 48:19 - Buku Lopatulika

19 Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Koma bambo wakeyo adakana nati, “Ndikudziŵa, mwana wanga, ndikudziŵa. Adzukulu a Manase adzakhalanso anthu otchuka, koma mng'ono wakeyu adzatchuka kupambana iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yaikulu ya anthu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Koma abambo ake anakana nati, “Ndikudziwa, mwana wanga, ndikudziwa. Adzukulu a iyeyunso adzakhala mtundu waukulu. Komabe mʼbale wake wamngʼonoyu adzakhala wamkulu kuposa iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yayikulu ya anthu.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 48:19
17 Mawu Ofanana  

Koma Ine, taona, pangano langa lili ndi iwe, ndipo udzakhala iwe atate wa khamu la mitundu.


Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.


Ndipo Isaki anakonda Esau, chifukwa anadya nyama yake ya m'thengo; koma Rebeka anakonda Yakobo.


mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.


Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Ejipito; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu;


Ndipo Israele anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pamutu wa Efuremu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lake lamanzere pamutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba.


Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pamutu wake.


Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efuremu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asiriya.


Apersiya, Aludi, Aputi, anali m'khamu lako; anthu ako a nkhondo anapachika chikopa ndi chisoti mwa iwe, anamveketsa kukoma kwako.


Yehova Mulungu wanu anakuchulukitsani, ndipo taonani, lero muchuluka ngati nyenyezi za kumwamba.


Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase.


Mwa fuko la Asere zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Nafutali zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Manase zikwi khumi ndi ziwiri.


Mwa fuko la Zebuloni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Yosefe zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Benjamini anasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa