Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 49:3 - Buku Lopatulika

3 Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga; ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga; ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 “Rubeni mwana wanga wachisamba, ndiwe nkhongono zanga, ndiwe mphatso yoyamba ya mphamvu zanga. Mwa ana anga onse, wopambana ndiwe pa ulemerero ndi mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 “Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa; mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga, wopambana pa ulemerero ndi mphamvu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 49:3
17 Mawu Ofanana  

Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.


Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:


ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;


Maina a ana a Israele amene anadza mu Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana aamuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.


Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pamutu wake.


Ana a Israele ndi awa: Rubeni, Simeoni, Levi, ndi Yuda, Isakara, ndi Zebuloni,


Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wake ukulu wake unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israele, koma m'buku la chibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wake.


ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele: Hanoki, ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi.


Ndipo Iye anapha achisamba onse m'dziko mwao, choyambira cha mphamvu yao yonse.


Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Ejipito, ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu.


Ndi m'malire a Efuremu, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Rubeni, limodzi.


Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israele, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;


Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israele; ana aamuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;


Koma azivomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lake la zake zonse; popeza iye ndiye chiyambi cha mphamvu yake; zoyenera woyamba kubadwa nzake.


Naimirire awa paphiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Asere, ndi Zebuloni, Dani ndi Nafutali.


Rubeni akhale ndi moyo, asafe, koma amuna ake akhale owerengeka.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikea lemba: Izi anena Ameni'yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa